25/08/2026
Mboni yachisanu ndi chitatu (8) pa mlandu wokupha Dr Victoria Bobe, Superintendent Lawrence Gondwe, omwe amagwira ntchito ku likulu la police ku Lilongwe ndipo amayang'anira zokhudza mfuti, ati malemuwa anawaombera ndi mfuti ya semi-automatic komanso pafupi.
Iwo ati izi ziri chomwechi chifukwa anapeza chipolopolo pamalo amene chiwembuchi chinachitikira komanso gun powder anamupeza pachitseko, m'mutu ndi pakhosi pa Dr Bobe.
A Gondwe akuyankha mafunso kuchokera kwa oyimira amene akuwaganizira mlanduwu, a Michael Goba Chipeta, ku bwalo la milandu lalikulu mu mzinda wa Blantyre.