13/01/2025
Nthawi zonse mkaziika mmalo mwawo ndimazazidwa mchisoni kuti iwowa "amamva bwanji?"
1.Munthu yemwe wagwera panjanje , theyalalo lachitsuloro ndikumuyenda pamutu ,onse kunyenyekeratu .Ngati umapweteka mwala ukagendedwa ,iwowaa zimawamvekera motani?π
2.Awo amene imfa zawo zinadzera kuzifwamba .Oyipayo mkusindikiza chikwanjecho pathupi lawo .Ngati kamawawa kampeni kodulira ndiwo kakakucheka ,iwowa amamva bwanji?π
3.Pakhomo kufika mlendo wolemekedzeka kwa iwo oti agona pompo ,koma mkukhala palibe chakudya,mkumangomuyan'gana.Amamva bwanji oyendeledwawo?π
4.Makamaka awo amene
adapedza chuma pathawi yomwe makolo onse adafa , pomwe iwowo adavutika ndi njala ,zimawamvekera motani ochipedzawo?π
6 kungodalitsa ukwatiwo ,kenako mmawa mwake mmodziyo imfa mkumampedza ,otsalayo zimamvekera motani?π
7.Kuphunzitsa mtsikana school kuti adzakwatirana;kenako njoleyo mkutengedwa ndi wina.Olipirayo amamva bwanji?π
8 Awo amene chiyambireni sanaonepo ,,sanayendepo ,kumva ngakhale kuyakhula .kwaiwo zimawamvekera motani?π
9 .Awo amene adafa kamba kamoto,thupi lonse kunyenyeka otsalawo mkutenga mphulusalo ngati umboni ,zimamveka bwanji?Nanga achibale awakufayo?π
10.Mtima sukukhadzikika makamaka mkaganiza za awo amene adakwiriridwa amoyo ,powasunga kuti apexe kaye malonda ,ngati timabanika tikatseka mphuno mwakanyengo iwowa amamva bwanji?
Osamangoti ndakumana ndimavuto ,anzanu adakumana mzoopsa kuposa zanuzo.
Bwanji osamangoyamika kwa Mlengiyo????????