14/08/2026
Nkhani za Masewero pa msika ogula ndi kugulitsana osewera ku Ulaya
🚨 TOTTENHAM IKUFUNA CODY GAKPO! ⚪⏳
Tottenham yayamba zokambirana ndi Liverpool zokhudza Cody Gakpo. Kusamukira kwake kupita ku timu ya Spurs kukuwoneka kuti ndi kotheka. 🇳🇱
ℹ️ Source: Plettigoal
🔴 RASHFORD WABWERERA KU SQUAD YA MAN UNITED!
Marcus Rashford waphatikizidwa mu squad ya osewera 26 a Manchester United pa masewera omaliza a pre-season ndi AC Milan. Akhoza kusewera koyamba Ku Manchester United kuyambira December 2024. 👀
ℹ️ Source: SamC_reports
🚨 NAPOLI IKUFUNA BADIASHILE!
Napoli ikukambirana ndi Chelsea za Benoit Badiashile. Chelsea ikufuna £25M, pomwe Napoli ikufuna mtengo wotsika.
(Source: The Sun Football)
🚨 CHELSEA IKUFUNA ALEX SCOTT NDI ADAM WHARTON!
Chelsea yayambanso kulumikizana ndi Bournemouth pa Alex Scott komanso Crystal Palace pa Adam Wharton. Scott akhoza kugulidwa ndi ndalama zoposa £80M.
(Source: TEAMtalk)
🚨 CHELSEA IKHOZA KUCHEPETSA MTENGO WA MALO GUSTO!
Chelsea ingachepetse mtengo wa Malo Gusto wa £75M ngati Liverpool itawonjezera chidwi chake pa defender wa ku France yi.
(Source: Siphillipssport)
🚨 CHELSEA IKUFUNA JJ GABRIEL WA MAN UNITED!
Chelsea ikufuna kusaina wonderkid wa Man United, JJ Gabriel, yemwe ali ndi zaka 15. United ikukambirana kale contract kuti isunge mnyamatayu, yemwe akufunidwanso ndi matimu akuluakulu ku Europe.
(Source: TEAMtalk)
🚨 COMO YAFUNSA ZA LIAM DELAP!
Como yapanga approach kwa Chelsea zokhudza Liam Delap. Striker-uyu ali pa mndandanda wa osewera omwe Como ikufuna.
(Source: Fabrizio Romano)
🚨 ARSENAL YAGWIRIZANA NDI VINCENT JOSEPH!
Arsenal yagwirizana ndi Liverpool pa osewera wawo wachichepere Vincent Joseph pa kusamukira ku Emirates. Komabe, matimuwa sanagwirizane pa ndalama zolipirira Liverpool.
(Source: The Athletic FC)
🚨 MAN UNITED SIKUFUNA KUGULITSA BRUNO FERNANDES!
Manchester United ilibe cholinga chogulitsa captain wake Bruno Fernandes. Akadali wofunika kwambiri pa mapulani a Michael Carrick ndipo akufuna kupitiriza ku Old Trafford.
(Source: TEAMtalk)
🚨 ARSENAL IKUFUNA JARELL QUANSAH!
Arsenal ikufuna defender wa Bayer Leverkusen, Jarell Quansah. Ikuyang'ananso Ezri Konsa wa Aston Villa ndi Jacobo Ramón wa Como.
(Source: Sky Sports)
🚨 MAN UNITED YAYANDIKIRA KUSAINA LOUIS PAGE!
Manchester United yagwirizana mwachinsinsi pa deal ya pafupifupi £10M ya Louis Page wa Leicester City. Zatsala kumaliza zinthu zochepa.
(Source: Intexcl)
🚨 ASTON VILLA IKUFUNA PALHINHA NDI WAN-BISSAKA!
Aston Villa ikufuna João Palhinha wa Bayern Munich komanso Aaron Wan-Bissaka wa West Ham kuti ilimbikitse squad yake.
(Source: The Times)
🚨 BARCOLA AKUYANDIKIRA KUPITA KU LIVERPOOL!
Liverpool ikuyandikira kusaina Bradley Barcola wa PSG pa ndalama zokwana €125M. Akhoza kusaina contract mpaka 2032.
(Source: Nicolo Schira)
🚨 ATLETICO SIKUFUNA JULIAN ALVAREZ APITE KU BARCELONA!
Atlético Madrid yakana kulola Julian Alvarez kupita ku Barcelona. Ngati achoka ku Spain, Arsenal ikuonedwa ngati yomwe ili patsogolo pomufuna.
(Source: ElNacional.cat)
🚨 ARSENAL IKUFUNA MARC PUBILL!
Mikel Arteta akufuna Marc Pubill, koma Atlético Madrid yanena kuti defender-uyu si wogulitsa ndipo dealyi pano ndi yovuta.
(Source: Diario AS)
🚨 ARSENAL IKUKANKHIRA KUSAINA OSIMHEN!
Victor Osimhen ndi target nambala wani wa Mikel Arteta pa gawo lotsala la transfer window. Arsenal ikufuna kumaliza dealyi deadline isanakwane.
(Source: Sebnonda)
🚨 TOTTENHAM YAPEREKA £85M PA SAVINHO!
Tottenham yapereka £85M kwa Manchester City pofuna kusaina Savinho. Koma City sikufuna kumugulitsa mosavuta, ngakhale wosewerayu akufuna kuchoka.
(Source: Cahemota)
💰 REIJNDERS AKUPITA KU AL-QADSIAH!
Tijjani Reijnders akuyembekezeka kupeza €100M pa zaka zisanu akapita ku Al-Qadsiah, zomwe ndi pafupifupi €385,000 pa sabata.
(Source: Mike Verweij)
🚨 BARCELONA IKUFUNA LUIS SUÁREZ NGATI ALVAREZ ALEPHELE KUMUSAINA
Barcelona ikuona Luis Suárez wa Sporting ngati njira ina ngati yalephera kusaina Julian Alvarez.
(Source: Fabrizio Romano)
🚨 PSG YAGWIRIZANA NDI AJAX PA MIKA GODTS!
PSG ndi Ajax agwirizana pa deal yosaina Mika Godts pandalama zokwana €55M. Zikalata zikuyembekezeka kusainidwa.
(Source: Fabrizio Romano)
🚨 DARWIN NÚÑEZ AKUPITA KU TRABZONSPOR!
Darwin Núñez akupita ku Trabzonspor pa loan ya season imodzi kuchokera ku Al Hilal. Trabzonspor yapambana mpikisano ndi Beşiktaş wolimbirana osewerayi.
(Source: Sacha Tavolieri)
🚨 FRED AKUBWERERA KU BRAZIL!
Atlético Mineiro yagwirizana ndi Fenerbahçe pa Fred. Deal ndi €2M kuphatikiza €500K ya ma bonus, ndipo asayina mpaka 2030.
(Source: Fabrizio Romano)
🚨 BARCELONA IKUFUNA RODRI!
Barcelona yapereka €55M kuphatikiza ma bonus mpaka €65M pa Rodri. Man City ikufuna €60M pomwepo kapena pafupifupi €70M kuphatikiza ma bonus. Pakadali pano kusiyana ndi pafupifupi €5M.
(Source: Mundo Deportivo)
🚨🔥 CHELSEA IKUKANA KUGULITSA ENZO FERNÁNDEZ!
Chelsea yati siyigulitsa Enzo Fernández ku Manchester City ndipo ikupitiriza kufuna £120M. City ikupitiriza kulumikizana ndi camp ya Enzo, ndipo maola otsalawa ndi ofunikira kwambiri pa dealyi.
(Source: Fabrizio Romano