ONANI

ONANI Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from ONANI, Legal, ONANI@gmail. com, Blantyre.

Zachitikanso ku Nigeria. Anthu anathamangira kukaba mafuta truck itawonongeka Saturday pa 18 January.Truck yaphulika. An...
20/01/2025

Zachitikanso ku Nigeria. Anthu anathamangira kukaba mafuta truck itawonongeka Saturday pa 18 January.

Truck yaphulika. Anthu 70 amwalira.

Matupi 60 apezeka pamene 10 aphyeratu.

 Bungwe la boma loona za milingo ya katundu la Malawi Bureau of Standards latseka malo atatu ogulitsiramo katundu a Sana...
20/01/2025


Bungwe la boma loona za milingo ya katundu la Malawi Bureau of Standards latseka malo atatu ogulitsiramo katundu a Sana mu mzinda wa Blantyre kaamba kosowa ukhondo komanso kusunga katundu yemwe masiku ake ogwilitsa ntchito anadutsa.

Mkulu woona zofalitsa mauthenga ku MBS a Wazamazama Katatu watsimikiza izi ponena kuti Sana yomwe ili mumsewa wa Limbe pafupi ndi malo okwelera ma bus opita ku Mulanje, ina yomwe ili pafupi ndi Agora mu Limbe komanso yaku Victoria Avenue ndiwo awatseka.

(by Cassim Aubi-Blantyre:01/20/2025)

16/01/2025

Apolisi ya Area 25 Junction Police Unit mu mzinda wa Lilongwe amanga mkulu wina yemwe akumuganizira kuti amafuna kubera wakabaza wa njinga yamoto.

Malingana ndi mneneri wa polisi ya Kanengo a Grisham Ngwira, mkuluyi a Alfred Chakwana a zaka 37, anatenga wakabazayu ku City Centre mu mzinda wa Lilongwe kupita naye ku Kanengo.

Anthuwa akuti anagwilizana ndithu pa mtengo wa 4000 kwacha, koma atafika ku Kanengo-ko mkuluyi akuti amachita zozengereza pa nkhani yopereka ndalama, ndipo anawuza wa kabazayo, kuti ayende pang'ono kufika pamalo pena pa zii kuti akampatse ndalamayo.

A Ngwira akuti mkangano unabuka pakati pa awiriwa, ndipo wapolisi wina yemwe amadutsa atamva izi, anagwira a mkulu oganizilidwayu, ndipo atamusecha anamupeza ndi mpeni.

Malingana ndi a Ngwira, oganizilidwayu amakakamira kuti amutengere wa kabazayu malo omwe atchuka ndi, mtchitidwe wa anthu ena omwe akumachita chipongwe a Kabaza.

(by InnocentKumchedwa-Lilongwe;15/01/25)

“I wonder what Burna Boy for do that kind of fan” - X user references Wizkid over ODG fan outburst 🤔🤔🤔🚨🚨🚨🚨🍿🍿🍿
15/01/2025

“I wonder what Burna Boy for do that kind of fan” - X user references Wizkid over ODG fan outburst 🤔🤔🤔🚨🚨🚨🚨🍿🍿🍿

15/01/2025

Mfumu Mwanyanja yaphedwa poiganizira kuti ndi mfiti Malawi 24 | Latest News from Malawi | Stay up-to-date with the latest news from Malawi and around the world, 24/7.

Mfumu Mwanyanja yaphedwa poiganizira kuti ndi mfitiApolisi m'boma la Chitipa akhazikitsa ntchito yosakasaka amaliwongo o...
15/01/2025

Mfumu Mwanyanja yaphedwa poiganizira kuti ndi mfiti

Apolisi m'boma la Chitipa akhazikitsa ntchito yosakasaka amaliwongo osadziwika omwe apha mfumu Mwanyanja, m'dera la mfumu yaikulu Nthalire m'bomalo.

Werengani nkhani yonse apa:

Mfumu Mwanyanja yaphedwa poiganizira kuti ndi mfiti Malawi 24 | Latest News from Malawi | Stay up-to-date with the latest news from Malawi and around the world, 24/7.

 Kafukule Police in Mzimba District have arrested three Ethiopian nationals—Mubarike Temen (27), Salamuni Aman (18), and...
15/01/2025



Kafukule Police in Mzimba District have arrested three Ethiopian nationals—Mubarike Temen (27), Salamuni Aman (18), and Tsedeke Girma (18)—for illegally entering Malawi.

According to Kafukule Police publicist, Masiku Munyungwa, the suspects were apprehended on January 14, 2024, near Nshoni Village after locals reported an abandoned black Ford Everest with burst tires.

The vehicle's driver, who had been hiding the immigrants in a nearby bush, injured a villager with a panga knife before fleeing the scene.

Villagers confiscated his phone, driver’s license, and car keys, which have been handed over to the police to aid in the investigation.

The car owner, Thomas Simbeye, has also been taken into custody, and all suspects will face charges in court.

The police have commended the community for their cooperation and are continuing efforts to locate the driver. Meanwhile, the injured villager is receiving medical treatment.

Reported by Ephraim Mkali Banda

𝗭𝗔𝗡𝗬𝗘𝗡𝗚𝗢(Lachitatu pa 15 January 2025)Kukhala kwa mitambo, kufunda komanso kugwa mvula yamabingu m’madera ena yomwe igwe...
15/01/2025

𝗭𝗔𝗡𝗬𝗘𝗡𝗚𝗢
(Lachitatu pa 15 January 2025)

Kukhala kwa mitambo, kufunda komanso kugwa mvula yamabingu m’madera ena yomwe igwe ya mphamvu m’madera ena am’phepete mwa nyanja ya Malawi m’mawa uno.
Masana ano, kukhala kwa mitambo ndipo kutentha komanso kugwa mvula yomwe igwe ya mphamvu m’madera ena. Mphepo idziomba yamkuntho m’madera omwe mugwe mvula ya mabingu.

𝗖𝗵𝗶𝗱𝘇𝗶𝘄𝗶𝘁𝘀𝗼 𝗰𝗵𝗮 𝗡𝗮𝗺𝗼𝗻𝗱𝘄𝗲 𝗗𝗶𝗸𝗲𝗹𝗲𝗱𝗶
Nthambi yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikudziwitsa mtundu wa a Malawi kuti Namondwe Dikeledi akadali m’nyanja ya m’chere ya pakati pa maiko a Madagascar ndi Mozambique (Mozambique Channel) kufupi ndi mzinda wa Angoche ku chigawo cha Nampula pa mtunda wapafupifupi makilomita 460 kuchokera ku Malawi. Komabe, namondweyu wachepako mphamvu pang’ono ndipo tsopano ali pa mlingo wa 990hPa pomwe akupitiriza kuyenda ndi liwiro la makilomita 13 pa ola kumalowera kum’mwera chakuzambwe kwa nyanja ya mchere ya pakati pa Madagascar ndi Mozambique. Namondwe Dikeledi akuyembekezeka kukula mphamvu pofika mawa. Kuthekera kwakuti namondweyu angafike ku Malawi kuno ndi kochepa kwambiri. Komabe, namondweyu akuyembekezeka kulimbikitsa mvula m’madera ena a ku Malawi yomwe ikuyembekezeka kugwa yamphamvu m’madera ena. Nthambi yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ipitirira kutipatsira kauniuni wa momwe namondweyu akuyendera.

(Kuchokera ku Department of Climate Change and Meteorological Services)

Today, we honour the legacy of John Chilembwe, a true hero who stood for justice and freedom. His extraordinary courage ...
15/01/2025

Today, we honour the legacy of John Chilembwe, a true hero who stood for justice and freedom. His extraordinary courage inspires us to strive for a better future.

Address

ONANI@gmail. Com
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when ONANI posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category